Ntchito ya Kutapulusa Baibolo mu Chinsenga
Ntchito ya kutapulusa Baibolo mu chinsenga yeyamba mu Mwezi wa March 2010 ku Petauke, pa msonkhano wa magulu ngati Nsenga Bible Translation Project (NBTP) na Bible Society of Zambia (BSZ). Pambuyo pake, atsogoleri a mipingo, akulu a komiti, mafumu, na akulu a boma analowa nawo ntchito iyi.
Mu May 2010, Bible Society of Zambia anakumana na nthumwi za Lutheran Bible Translators (LBT). Mu May 2012, pa utsogoleri wa Bible Society of Zambia, anthu anakumana ku workshop ndipo atanthauzili atatu anasankhidwa. Ntchitoiyi yeyamba mwalamulo pa 1 July 2012.
Mu July 2015, ntchito ya ParaText yeyambika ndipo ntchito yosinthana zolemba ndi ma server a Bible Society nayonso yeyamba.
Mu August, Bible Society of South Korea inachita typesetting ya Nsenga New Testament. Kukhazikitsiwa kwa Baibolo la Chipangano Chatsopano kwechitika pa 14 July 2016 na thandizo linachokera ku United Bible Societies (UBS), Bible Society of Zambia (BSZ), Lutheran Bible Translators (LBT), na ETEN.
Mu January 2016, ntchito ya Chipangano Chakale yeyamba. Mu March 2021, chikalata choyamba chemalizidwa, koma DC Books sinalowe.
Ndi chisomo cha Mulungu, tikuyembekezera kumalizidwa kwake.